Categories
NUMERI

NUMERI 30

Za chowinda chochita akazi

1 Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi:

2 Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m’kamwa mwake.

3 Ndipo mkazi akachitira Yehova chowinda, nakadzimanga nacho chodziletsa, pokhala ali m’nyumba ya atate wake, mu unamwali;

4 ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga nacho moyo wake, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika.

5 Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.

6 Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zake, kapena zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake;

7 nakazimva mwamuna wake, nakakhala naye chete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zake zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.

8 Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.

9 Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira.

10 Ndipo ngati anawinda m’nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo,

11 ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.

12 Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m’milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; mwamuna wake anafafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira iye.

13 Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza.

14 Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye.

15 Koma akazifafaniza atatha kuzimva; pamenepo adzasenza mphulupulu yake.

16 Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m’nyumba ya atate wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/30-49281e6182ef3cdfb9dc3e40e89434a5.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *