Aisraele aononga Akanani
1 Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.
2 Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m’dzanja langa, ndidzaononga mizinda yao konse.
3 Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi mizinda yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.
Njoka yamkuwa
4 Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.
5 Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m’chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu.
6 Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israele.
7 Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.
8 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto, nuiike pa mtengo wake; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo.
9 Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.
Achoka kunka ulendo wao
10 Pamenepo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema mu Oboti.
11 Ndipo anachoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyeabarimu, m’chipululu chakuno cha Mowabu, kotulukira dzuwa.
12 Pochokapo anayenda ulendo, namanga mahema m’chigwa cha Zeredi.
13 Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m’chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori.
14 Chifukwa chake, ananena m’buku la Nkhondo za Yehova,
Waheba mu Sufa,
ndi miyendo ya Arinoni;
15 ndi zigwa za miyendoyo
zakutsikira kwao kwa Ari,
ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu.
16 Ndipo atachokapo anamuka ku Beere, ndicho chitsime chimene Yehova anachinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi.
17 Pamenepo Israele anaimba nyimbo iyi,
Tumphuka chitsime iwe;
muchithirire mang’ombe;
18 chitsime adakumba mafumu,
adachikonza omveka a anthu;
atanena mlamuli, ndi ndodo zao.
Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana;
19 atachoka ku Matana ku Nahaliyele; atachoka ku Nahaliyele ku Bamoti;
20 atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m’dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu.
Aisraele alanda dziko la Aamori
21 Ndipo Israele anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti,
22 Ndipitire pakati padziko lako; sitidzapatuka kulowa m’munda, kapena m’munda wampesa, sitidzamwako madzi a m’zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako.
23 Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m’malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m’chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele.
24 Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.
25 Ndipo Israele analanda mizinda iyi yonse; nakhala Israele m’mizinda yonse ya Aamori; mu Hesiboni ndi midzi yake yonse.
26 Popeza Hesiboni ndiwo mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m’dzanja lake kufikira Arinoni.
27 Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti,
Idzani ku Hesiboni,
mzinda wa Sihoni umangike, nukhazikike.
28 Popeza moto unatuluka mu Hesiboni,
chirangali cha moto m’mzinda wa Sihoni;
chatha Ari wa Mowabu,
eni misanje ya Arinoni.
29 Tsoka kwa iwe, Mowabu!
Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu,
anapereka ana ake aamuna opulumuka,
ndi ana ake aakazi akhale ansinga,
kwa Sihoni mfumu ya Aamori.
30 Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni,
ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa.
Ndiwo wakufikira ku Medeba.
31 Chomwecho Israele anakhala m’dziko la Aamori.
32 Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda midzi yake, napirikitsa Aamori a komweko.
Aisraele alanda dziko la Basani
33 Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya ku Basani anatuluka kukumana nao, iye ndi anthu ake onse, kudzachita nao nkhondo ku Ederei.
34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m’manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.
35 Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/21-153816cdf374f671075357116b766512.mp3?version_id=1068—