Za ng’ombe yaikazi yofiira ndi madzi oyeretsa nao
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2 Ili ndi lemba la chilamulo Yehova adalamulirachi, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele kuti azikutengera ng’ombe yaikazi yofiira, yangwiro yopanda chilema, yosamanga m’goli;
3 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake.
4 Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pachihema chokomanako.
5 Pamenepo atenthe ng’ombe yaikaziyo pamaso pake; atenthe chikopa chake ndi nyama yake, ndi mwazi wake, pamodzi ndi chipwidza chake.
6 Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndihisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng’ombe yaikazi.
7 Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
8 Ndipo iye wakutentha ng’ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
9 Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng’ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m’malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo.
10 Ndipo wakuola mapulusayo a ng’ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.
11 Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;
12 iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri.
13 Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa chihema cha Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye.
14 Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m’hema, yense wakulowa m’hemamo, ndi yense wakukhala m’hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.
15 Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa.
16 Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.
17 Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yauchimo, nathirepo m’chotengera madzi oyenda;
18 ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m’madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.
19 Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m’madzi, nadzakhala woyera madzulo.
20 Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.
21 Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
22 Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/19-f0ea25e1a90155dc929b1d78188541aa.mp3?version_id=1068—