Malamulo a pa nsembezo
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,
2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mukakalowa m’dziko lokakhalamo inu, limene ndilikupatsa inu,
3 ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng’ombe kapena nkhosa;
4 pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta;
5 ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wamwanawankhosammodzi.
6 Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini.
7 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo atatu la hini, achitire Yehova fungo lokoma.
8 Ndipo pamene mukonza ng’ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;
9 abwere nayo, pamodzi ndi ng’ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosakaniza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini.
10 Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova.
11 Kudzatero ndi ng’ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense.
12 Monga mwa kuwerenga kwake kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwake.
13 Onse akubadwa m’dzikomo achite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma.
14 Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso,
15 Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.
16 Pakhale chilamulo chimodzi ndi chiweruzo chimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.
17 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
18 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene mulowa m’dziko limene ndilikukulowetsani,
19 kudzali, pakudya inu mkate wa m’dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza.
20 Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumachitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza,
21 Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.
22 Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose;
23 ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova analamula, ndi kunkabe m’mibadwo yanu;
24 pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng’ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.
25 Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala.
26 Ndipo khamu lonse la ana a Israele, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linachichita osati dala.
27 Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo.
28 Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa.
29 Kunena za wobadwa m’dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala.
30 Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m’dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.
31 Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lake; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yake ikhale pa iye.
Alangidwa wosasunga Sabata
32 Ndipo pokhala ana a Israele m’chipululu, anapeza munthu wakufuna nkhuni tsiku laSabata.
33 Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.
34 Ndipo anayamba wamsunga, popeza sichinanenedwe choyenera kumchitira iye.
35 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa chigono.
36 Pamenepo khamu lonse linamtulutsa kunja kwa chigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose.
Pakhale chizindikiro pa zovala zao
37 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
38 Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m’mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m’mphepetemo thonje lamadzi.
39 Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang’anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m’mtima mwanu, ndi za m’maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;
40 kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu.
41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakukutulutsani m’dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/15-9d0140c4b5be3255e8abd33f2cd93ab6.mp3?version_id=1068—