Categories
NUMERI

NUMERI 12

Miriyamu ndi Aroni aukira Mose

1 Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.

2 Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga? Ndipo Yehova anamva.

3 Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.

4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza kuchihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo.

5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri.

6 Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhalamneneripakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m’masomphenya, ndinena naye m’kulota.

7 Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m’nyumba mwanga monse.

8 Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.

9 Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye.

10 Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.

11 Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako.

12 Asakhaletu iye ngati wakufa, amene dera lina la mnofu wake watha potuluka iye m’mimba mwa make.

13 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mchiritsenitu, Mulungu.

14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.

15 Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu.

16 Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m’chipululu cha Parani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/12-642d409a0d6a8b7aa744c1537788ef5e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *