Adzipangira malipenga awiri asiliva
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m’zigono.
3 Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo lachihema chokomanako.
4 Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a mu Israele, azisonkhana kuli iwe.
5 Mukaliza chokweza ayende a m’zigono za kum’mawa.
6 Mukalizanso chokweza, a m’zigono za kumwera ayende; alize chokweza pakumuka.
7 Pomemeza msonkhano mulize, wosati chokweza ai.
8 Ana aamuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu.
9 Ndipo pamene mupita kunkhondo m’dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.
10 Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Aisraele achoka ku Sinai
11 Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa chihema cha mboni.
12 Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m’chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m’chipululu cha Parani.
13 Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
14 Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang’anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.
15 Ndi pa gulu la fuko la ana a Isakara panali Netanele mwana wa Zuwara.
16 Ndi gulu la fuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni.
17 Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.
18 Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang’anira Elizuri mwana wa Sedeuri.
19 Ndi pa gulu la fuko la ana a Simeoni anayang’anira Selumiele mwana wa Zurishadai.
20 Ndi pa gulu la fuko la ana a Gadi anayang’anira Eliyasafu mwana wa Deuwele.
21 Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.
22 Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang’anira Elisama mwana wa Amihudi.
23 Ndi pa gulu la fuko la ana a Manase anayang’anira Gamaliele mwana wa Pedazuri.
24 Ndi pa gulu la fuko la ana a Benjamini anayang’anira Abidani mwana wa Gideoni.
25 Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m’mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang’anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
26 Ndi pa gulu la fuko la ana a Asere anayang’anira Pagiyele mwana wa Okarani.
27 Ndi pa gulu la fuko la ana a Nafutali anayang’anira Ahira mwana wa Enani.
28 Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao.
Mose apempha Hobabu awaperekeze
29 Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
30 Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga.
31 Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m’chipululu, ndipo udzakhala maso athu.
32 Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma zilizonse Yehova atichitira ife, zomwezo tidzakuchitira iwe.
33 Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipolikasa la chipanganocha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.
34 Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono.
35 Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu.
36 Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/10-32ca20667530fb06da5fd7ec8e3acae1.mp3?version_id=1068—