Msonkhano wa kusala ndi kupemphera
1 Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndikuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi.
2 Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.
3 Naimirira poima pao, nawerenga m’buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao.
4 Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau aakulu kwa Yehova Mulungu wao.
5 Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
6 Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m’mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.
7 Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa mu Uri wa kwa Akaldeya, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu;
8 ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.
9 Ndipo munapenya msauko wa makolo athu mu Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira,
10 nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsaFaraondi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m’dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.
11 Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m’madzi olimba.
12 Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m’njira akayendamo.
13 Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
14 ndiSabatalanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
15 ndi mkate wochokera m’mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m’thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.
16 Koma iwo ndi makolo athu anachita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu,
17 nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m’kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.
18 Ngakhale apa atadzipangira mwanawang’ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu;
19 koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m’chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m’njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
20 Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamanemanaanu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.
21 Ndipo munawalera zaka makumi anai m’chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinathe, ndi mapazi ao sanatupe.
22 Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m’madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.
23 Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m’mwamba, nimunawalowetsa m’dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao.
24 Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m’dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m’dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m’dziko, kuti achite nao chifuniro chao.
25 Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda yaazitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.
26 Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m’mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
27 Chifukwa chake munawapereka m’dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m’dzanja la adani ao.
28 Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m’dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva mu Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;
29 ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.
30 Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m’dzanja la mitundu ya anthu a m’dziko.
31 Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawathe, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo.
32 Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.
33 Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa;
34 ndi mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunge chilamulo chanu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawachitira umboni nazo.
35 Popeza sanatumikire Inu mu ufumu wao, ndi mu ubwino wanu wochuluka umene mudawapatsa, ndi m’dziko lalikulu ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerere kuleka ntchito zao zoipa.
36 Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zake ndi zokoma zake, taonani, ife ndife akapolo m’menemo.
37 Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu.
38 Ndipo mwa ichi chonse tichita pangano lokhazikika, ndi kulilemba, ndi akulu athu, Alevi athu, ndi ansembe athu, alikhomera chizindikiro.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/9-c7809a61e3fe57e74c91cf1d3f4e9932.mp3?version_id=1068—