Adani ayesa kunyenga ndi kuopsa Nehemiya
1 Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata);
2 anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa.
3 Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
4 Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo.
5 Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wake kwa ine kachisanu, ndi kalata yosatseka m’dzanja mwake;
6 m’menemo mudalembedwa, Kwamveka mwaamitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa.
7 Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe kuYerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.
8 Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako.
9 Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano.
10 Pamenepo ndinalowa m’nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m’kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe.
11 Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa mu Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo.
12 Ndipo ndinazindikira kuti sanamtume Mulungu; koma ananena choneneracho pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera.
13 Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.
14 Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiyamneneriwamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.
15 Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.
16 Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu.
17 Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso makalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso makalata ake a Tobiya.
18 Pakuti ambiri mu Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya.
19 Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza makalata kuti andiopse ine.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/6-008ca1ec27add51061ee2ed3de4c9646.mp3?version_id=1068—