Categories
NAHUMU

NAHUMU 3

Zoipa za Ninive ndi kupasuka kwake

1 Tsoka mzinda wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza.

2 Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta;

3 munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong’anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

4 chifukwa cha chiwerewere chochuluka cha wachiwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsaamitundumwa chiwerewere chake, ndi mabanja mwa nyanga zake.

5 Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako.

6 Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo.

7 Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza?

8 Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pamtsinje wozingidwa ndi madzi; amene tchemba lake ndilo nyanja, ndi linga lake ndilo nyanja?

9 Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza.

10 Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo.

11 Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira chifukwa cha mdani.

12 Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m’kamwa mwa wakudya.

13 Taona, anthu ako m’kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako.

14 Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng’anjo yanjerwa.

15 Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe.

16 Wachulukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; chirimamine anyambita, nauluka, nathawa.

17 Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazembe ako ngati ziwalamsatsi zakutera m’matchinga tsiku lachisanu, koma likatuluka dzuwa ziuluka ndi kuthawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.

18 Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.

19 Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NAM/3-3ee4e47dfc76afa9f7c724171064fb7f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *