Categories
NAHUMU

NAHUMU 1

Chilungamo ndi chifundo cha Mulungu. Adzaononga adani ndi kulanditsa anthu ake

1 Katundu wa Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.

2 Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera chilango; Yehova ndiye wobwezera chilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera chilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ake.

3 Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m’kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.

4 Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basani ndi Karimele afota, ndi duwa la ku Lebanoni linyala.

5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m’mwemo.

6 Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.

7 Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

8 Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima.

9 Mulingaliranji chotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

10 Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.

11 Mwa iwe watuluka wina wolingalira choipa chotsutsana ndi Yehova, ndiye phungu wopanda pake.

12 Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nachuluka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Chinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.

13 Koma tsopano ndidzathyola ndi kukuchotsera goli lake, ndipo ndidzadula zomangira zako.

14 Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m’nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.

15 Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NAM/1-9e429d61b8c465db9f9a40f9abc7a2ae.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *