Ngakhale Mulungu apatsa munthu zonse azikhumba koma mtima sukhuta nazo
1 Pali choipa ndachiona kunja kuno chifalikira mwa anthu,
2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.
3 Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;
4 pakuti ikudza mwachabe, nichoka mumdima, mdima nukwirira dzina lake.
5 Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;
6 akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi?
7 Ntchito zake zonse munthu angogwirira m’kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta.
8 Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?
9 Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
10 Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu.
11 Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?
12 Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m’tsogolo mwake kunja kuno?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/6-36290b2c86cc0e37329dd7049368d6a2.mp3?version_id=1068—