Categories
MLALIKI

MLALIKI 5

Malangizo osiyana akuwasamalira anthu m’moyo uno

1 Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.

2 Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.

3 Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito; ndipo mau a chitsiru mwakuchuluka maneno.

4 Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.

5 Kusawinda kupambana kuwinda osachita.

6 Usalole m’kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?

7 Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.

8 Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.

9 Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza;

10 Wokondasilivasadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.

11 Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?

12 Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.

13 Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;

14 koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m’dzanja lake mulibe kanthu.

15 Monga anatuluka m’mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m’dzanja lake.

16 Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?

17 Inde masiku ake onse amadya mumdima, ndipo zimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.

18 Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.

19 Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.

20 Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wake kwambiri; chifukwa Mulungu amvomereza m’chimwemwe cha mtima wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/5-496d7a038ca21e3be0705ca3db35eaa1.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *