Zilizonse zili ndi nyengo yake, Mulungu ndi kuziika zonse
1 Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;
2 mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo;
3 mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;
4 mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina;
5 mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;
6 mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;
7 mphindi yakung’amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;
8 mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.
9 Wogwira Ntchito aona phindu lanji m’chomsautsacho?
10 Ndaona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo.
11 Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.
12 Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo.
13 Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.
14 Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake.
15 Chomwe chinaoneka, chilikuonekabe; ndi chomwe chidzaoneka chinachitidwa kale; Mulungu anasanthula zochitidwa kale.
16 Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.
17 Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.
18 Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zichitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ake kuti ndiwo nyama zakuthengo.
19 Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe.
20 Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.
21 Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?
22 M’mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/3-8e358d8041764b8562c5445f8022c926.mp3?version_id=1068—