Categories
MLALIKI

MLALIKI 2

Za m’moyo uno sizitha kukondweretsa mtima

1 Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.

2 Ndinati, Kuseka ndi masala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?

3 Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.

4 Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa;

5 ndinakonza mphanje ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundumitundu;

6 ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m’nkhalango momeramo mitengo;

7 ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing’ono kupambana onse anakhala muYerusalemundisanabadwe ine;

8 ndinakundikansosilivandi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.

9 Ndinakula chikulire kupambana onse anali mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.

10 Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamane; sindinakanize mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m’ntchito zanga zonse ndi limeneli.

11 Pamenepo ndinayang’ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.

12 Ndipo ndinatembenuka kukayang’ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale.

13 Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.

14 Wanzeru maso ake ali m’mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.

15 Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.

16 Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m’tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.

17 Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

18 Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzamsiyira izo munthu wina amene adzanditsata.

19 Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.

20 Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za ntchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.

21 Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.

22 Pakuti munthu ali ndi chiyani m’ntchito zake zonse, ndi m’kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno?

23 Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndi chabe.

24 Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.

25 Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.

26 Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/2-7e1af7472df83fb66d8bdf327a368b14.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *