Categories
MLALIKI

MLALIKI 11

Tizichita zokoma lero lino posadziwa za mawa

1 Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.

2 Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano.

3 Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwera pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.

4 Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.

5 Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m’mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.

6 Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.

7 Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m’kuona dzuwa.

8 Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzachuluka. Zonse zilinkudza zili zachabe.

Anyamata asangalale, koma adzikonzeretu pokumbukira imfa ikudza

9 Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.

10 Chifukwa chake chotsani zopweteka m’mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/11-490240226c1c1418d83865f9ce75f2a3.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *