Za pansi pano nzachabe
1 Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya muYerusalemu.
2 Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.
3 Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?
4 Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.
5 Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako.
6 Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.
7 Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
8 Zinthu zonse zilemetsa; munthu sangathe kuzifotokoza; maso sakhuta m’kuona, ndi makutu sakhuta m’kumva.
9 Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.
10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.
11 Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m’tsogolomo, sadzazikumbukirai.
12 Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele mu Yerusalemu.
13 Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14 Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
15 Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe.
16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.
17 Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.
18 Pakuti m’nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ECC/1-dd0ec0fb2ee2fa728bfb140a46f68729.mp3?version_id=1068—