Madyerero a Nzeru
1 Nzeru yamanga nyumba yake,
yasema zoimiritsa zake zisanu ndi ziwiri;
2 yaphera nyama yake, nisakaniza vinyo wake,
nilongosolanso pa gome lake.
3 Yatuma anamwali ake, iitana
pa misanje ya m’mudzi.
4 Wazibwana yense apatukire kuno;
iti kwa yense wosowa nzeru,
5 Tiyeni, idyani chakudya changa;
nimumwe vinyo wanga ndamsakaniza.
6 Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo;
nimuyende m’njira ya nzeru.
7 Woweruza munthu wonyoza adzichititsa yekha manyazi;
yemwe adzudzula wochimwa angodetsa mbiri yakeyake.
8 Usadzudzule wonyoza kuti angakude;
dzudzula wanzeru adzakukonda.
9 Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake;
ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira.
10 Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova;
kudziwa Woyerayo ndiko luntha.
11 Pakuti mwa ine masiku ako adzachuluka,
zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.
12 Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo?
Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.
13 Utsiru umalongolola,
ngwa chibwana osadziwa kanthu.
14 Ukhala pa khomo la nyumba yake,
pampando pa misanje ya m’mudzi,
15 kuti uitane akupita panjira,
amene angonkabe m’kuyenda kwao,
16 wachibwana ndani? Apatukire kuno.
Ati kwa yense wopanda nzeru,
17 madzi akuba atsekemera,
ndi chakudya chobisika chikoma.
18 Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko;
omwe achezetsa utsiru ali m’manda akuya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/9-f14cb55a6d54b6ebae11a55edb662d4b.mp3?version_id=1068—