Achenjere naye mkazi woipa
1 Mwananga, sunga mau anga,
ukundike malangizo anga,
2 Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo;
ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.
3 Uwamange pa zala zako,
uwalembe pamtima pako.
4 Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongo wanga;
nutche luntha mbale wako.
5 Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere,
kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake.
6 Pakuti pa zenera la nyumba yanga
ndinapenyera pamwamba pake;
ndinaona pakati pa achibwana,
7 ndinazindikira pakati pa aang’ono
mnyamata wopanda nzeru,
8 alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo,
ndi kuyenda panjira ya kunyumba yake;
9 pa madzulo kuli sisiro,
pakati pa usiku pali mdima.
10 Ndipo taona, mkaziyo anamchingamira,
atavala zadama wochenjera mtima,
11 ali wolongolola ndi wosaweruzika,
mapazi ake samakhala m’nyumba mwake.
12 Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo,
nabisalira pa mphambano zonse.
13 Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona;
nati kwa iye ndi nkhope yachipongwe,
14 nsembe zamtendere zili nane;
lero ndachita zowinda zanga.
15 Chifukwa chake ndatuluka kudzakuchingamira,
kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.
16 Ndayala zofunda pakama panga,
nsalu zamawangamawanga za thonje la ku Ejipito,
17 ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira amure
ndi chisiyo ndi sinamoni.
18 Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamawa;
tidzisangalatse ndi chiyanjano.
19 Pakuti mwamuna kulibe kwathu,
wapita ulendo wa kutali;
20 watenga thumba la ndalama m’dzanja lake,
tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.
21 Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake,
ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.
22 Mnyamatayo amtsata posachedwa,
monga ng’ombe ipita kukaphedwa;
ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru;
23 mpaka muvi ukapyoza mphafa yake;
amtsata monga mbalame yothamangira msampha;
osadziwa kuti adzaononga moyo wake.
24 Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,
labadirani mau a m’kamwa mwanga.
25 Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo,
usasochere m’mayendedwe ake.
26 Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa;
ndipo ophedwa ndi iye achulukadi.
27 Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda,
yotsikira kuzipinda za imfa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/7-27422fd7823f7b616ef37a976cfa2d76.mp3?version_id=1068—