Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 5

Achenjere naye mkazi woipa

1 Mwananga, mvera nzeru yanga;

tcherera makutu ku luntha langa;

2 ukasunge zolingalira,

milomo yako ilabadire zomwe udziwa.

3 Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi;

m’kamwa mwake muti see koposa mafuta.

4 Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo,

ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse.

5 Mayendedwe ake atsikira kuimfa;

mapazi ake aumirira kumanda;

6 sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;

mayendedwe ake adzandira dzandidzandi osadziwa iye.

7 Ndipo tsopano ana, mundimvere,

musapatuke ku mau a m’kamwa mwanga.

8 Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo,

osayandikira ku khomo la nyumba yake;

9 kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,

ndi zaka zako kwa ankhanza;

10 kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,

ndi kuti usagwire ntchito m’nyumba ya wachilendo;

11 ungalire pa chimaliziro chako,

pothera nyama yako ndi thupi lako;

12 ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,

mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo;

13 ndipo sindinamvere mau a aphunzitsi anga;

ngakhale kutcherera makutu kwa akundilanga mwambo!

14 Ndikadakhala m’zoipa zonse,

m’kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.

15 Imwa madzi a m’chitsime mwako,

ndi madzi oyenda a m’kasupe mwako.

16 Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,

ndi mitsinje ya madzi m’makwalala?

17 Ikhale ya iwe wekha,

si ya alendo okhala nawe ai.

18 Adalitsike kasupe wako;

ukondwere ndi mkazi wokula nayo.

19 Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo,

maere ake akukwanire nthawi zonse;

ukodwe ndi chikondi chake osaleka.

20 Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere,

ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo?

21 Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova,

asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.

22 Zoipa zakezake zidzagwira woipa;

adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake.

23 Adzafa posowa mwambo;

adzasochera popusa kwambiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/5-bbbe90f0618659e9199c566ac200b145.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *