Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 4

Chenjezo lakuti afune Nzeru nalewe njira za oipa

1 Ananu, mverani mwambo wa atate,

nimutchere makutu mukadziwe luntha;

2 pakuti ndikuphunzitsani zabwino;

musasiye chilangizo changa.

3 Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,

wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina.

4 Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,

mtima wako uumirire mau anga;

sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.

5 Tenga nzeru, tenga luntha;

usaiwale, usapatuke pa mau a m’kamwa mwanga;

6 usasiye nzeru, ndipo idzakusunga;

uikonde, idzakutchinjiriza.

7 Nzeru ipambana, tatenga nzeru;

m’kutenga kwako konseko utenge luntha.

8 Uilemekeze, ndipo idzakukweza;

idzakutengera ulemu pamene uifungatira.

9 Idzaika chisada cha chisomo pamutu pako;

idzakupatsa korona wokongola.

10 Tamvera mwananga, nulandire mau anga;

ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka.

11 Ndakuphunzitsa m’njira ya nzeru,

ndakuyendetsa m’mayendedwe olungama.

12 Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;

ukathamanga, sudzaphunthwa.

13 Gwira mwambo, osauleka;

uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.

14 Usalowe m’mayendedwe ochimwa,

usayende m’njira ya oipa.

15 Pewapo, osapitamo;

patukapo, nupitirire.

16 Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona;

ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.

17 Pakuti amadya chakudya cha uchimo,

namwa vinyo wa chifwamba.

18 Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha,

kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.

19 Njira ya oipa ikunga mdima;

sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.

20 Mwananga, tamvera mau anga;

tcherera makutu ku zonena zanga.

21 Asachoke kumaso ako;

uwasunge m’kati mwa mtima wako.

22 Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,

nalamitsa thupi lao lonse.

23 Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;

pakuti magwero a moyo atulukamo.

24 Tasiya m’kamwa mokhota,

uike patali milomo yopotoka.

25 Maso ako ayang’ane m’tsogolo,

zikope zako zipenye moongoka.

26 Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;

njira zako zonse zikonzeke.

27 Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere;

suntha phazi lako kusiya zoipa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/4-4bebf0641029010d0e0755c15bc99f54.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *