Malangizo a kuopa, kukhulupirira, ndi kumvera Yehova
1 Mwananga, usaiwale malamulo anga,
mtima wako usunge malangizo anga;
2 pakuti adzakuonjezera masiku ambiri,
ndi zaka za moyo ndi mtendere.
3 Chifundo ndi choonadi zisakusiye;
uzimange pakhosi pako;
uzilembe pamtima pako;
4 motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino,
pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5 Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse,
osachirikizika pa luntha lako;
6 umlemekeze m’njira zako zonse,
ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
7 Usadziyese wekha wanzeru;
opa Yehova, nupatuke pazoipa;
8 mitsempha yako idzalandirapo moyo,
ndi mafupa ako uwisi.
9 Lemekeza Yehova ndi chuma chako,
ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;
10 motero nkhokwe zako zidzangoti thee,
mbiya zako zidzasefuka vinyo.
11 Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova,
ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake;
12 pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda;
monga atate mwana amene akondwera naye.
Phindu la Nzeru
13 Wodala ndi wopeza nzeru,
ndi woona luntha;
14 pakuti malonda a nzeru aposa malonda asiliva,
phindu lake liposa golide woyengeka.
15 Mtengo wake uposa ngale;
ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.
16 Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake;
chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere.
17 Njira zake zili zokondweretsa,
mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.
18 Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira;
wakuiumirira ngwodala.
19 Yehova anakhazika dziko ndi nzeru;
naika zamwamba ndi luntha.
20 Zakuya zinang’ambika ndi kudziwa kwake;
thambo ligwetsa mame.
21 Mwananga, zisachokere kumaso ako;
sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;
22 ndipo mtima wako udzatengapo moyo,
ndi khosi lako chisomo.
23 Pompo udzayenda m’njira yako osaopa,
osaphunthwa phazi lako.
24 Ukagona, sudzachita mantha;
udzagona tulo tokondweretsa.
25 Usaope zoopsa zodzidzimutsa,
ngakhale zikadza zopasula oipa;
26 pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako,
nadzasunga phazi lako lingakodwe.
Malangizo ena osiyana
27 Oyenera kulandira zabwino usawamane;
pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.
28 Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso,
ndipo mawa ndidzakupatsa;
pokhala uli nako kanthu.
29 Usapangire mnzako chiwembu;
popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.
30 Usakangane ndi munthu chabe,
ngati sanakuchitire choipa.
31 Usachitire nsanje munthu wachiwawa;
usasankhe njira yake iliyonse.
32 Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova;
koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.
33 Yehova atemberera za m’nyumba ya woipa;
koma adalitsa mokhalamo olungama.
34 Anyozadi akunyoza,
koma apatsa akufatsa chisomo.
35 Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao;
koma opusa adzakweza manyazi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/3-e517f48ff8327cd8228c94a3e6c5b797.mp3?version_id=1068—