1 Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri;
kukukomera mtima anzako kuposasilivandi golide.
2 Wolemera ndi wosauka akumana,
wolenga onsewo ndiye Yehova.
3 Wochenjera aona zoipa, nabisala;
koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.
4 Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova
ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.
5 Minga ndi misampha ili m’njira ya wokhota;
koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.
6 Phunzitsa mwana poyamba njira yake;
ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.
7 Wolemera alamulira osauka;
ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.
8 Wofesa zosalungama adzakolola tsoka;
ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.
9 Mwini diso lamataya adzadala;
pakuti apatsa osauka zakudya zake.
10 Ukainga wonyoza, makangano adzatuluka;
makani ndi manyazi adzalekeka.
11 Wokonda kuyera mtima,
mfumu idzakhala bwenzi lake
chifukwa cha chisomo cha milomo yake.
12 Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa;
koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.
13 Waulesi ati, Pali mkango panjapo,
ndidzaphedwa pamakwalalapo.
14 M’kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya;
yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.
15 Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana;
koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.
16 Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake,
ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.
Malangizo a pa makhalidwe oyenera munthu
17 Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru,
nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.
18 Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m’kati mwako,
ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.
19 Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi,
kuti ukhulupirire Yehova.
20 Kodi sindinakulembere zoposa
za uphungu ndi nzeru;
21 kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona,
nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?
22 Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi,
ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.
23 Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao;
omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.
24 Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga;
ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;
25 kuti ungaphunzire mayendedwe ake,
ndi kutengera moyo wako msampha.
26 Usakhale wodulirana mpherere,
ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake.
27 Ngati ulibe chobwezera
kodi achotserenji kama lako pansi pako?
28 Usasunthe chidziwitso chakale cha m’malire,
chimene makolo ako anachiimika.
29 Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake?
Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/22-5349935a35273ed6009f979506c51d4f.mp3?version_id=1068—