Categories
MIYAMBO

MIYAMBO 21

1 Mtima wa mfumu uli m’dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi;

aulozetsa komwe afuna.

2 Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake;

koma Yehova ayesa mitima.

3 Kuchita chilungamo ndi chiweruzo

kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

4 Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,

ndi nyali ya oipa, zili tchimo.

5 Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu;

koma yense wansontho angopeza umphawi.

6 Kupata chuma ndi lilime lonama

ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

7 Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola;

chifukwa akana kuchita chiweruzo.

8 Wosenza tchimo njira yake ikhotakhota;

koma ntchito ya woyera mtima ilungama.

9 Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika

kuposa kukhala m’nyumba ndi mkazi wolongolola.

10 Wamphulupulu mtima wake umkhumba zoipa;

sakomera mtima mnzake.

11 Polangidwa wonyoza, wachibwana alandira nzeru,

naphunzira pakuyang’ana pa wanzeru.

12 Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu,

kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.

13 Wotseka makutu ake polira waumphawi,

nayenso adzalira koma osamvedwa.

14 Mphatso ya m’tseri ipembedza mkwiyo,

ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.

15 Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama;

koma kuwaononga akuchita mphulupulu.

16 Munthu wosochera panjira ya nzeru

adzakhala m’msonkhano wa akufa.

17 Wokonda zoseketsa adzasauka;

wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

18 Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama;

ndipo wachiwembu adzalowa m’malo mwa oongoka mtima.

19 Kukhala m’chipululu kufunika

kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong’ung’udza.

20 Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;

koma wopusa angozimeza.

21 Wolondola chilungamo ndi chifundo

apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.

22 Wanzeru akwera pa mzinda wa olimba,

nagwetsa mphamvu yake imene anaikhulupirira.

23 Wosunga m’kamwa mwake ndi lilime lake

asunga moyo wake kumavuto.

24 Wonyada wodzikuza dzina lake ndiye wonyoza;

achita mwaukali modzitama.

25 Chifuniro cha waulesi chimupha;

chifukwa manja ake akana kugwira ntchito.

26 Ena asirira modukidwa tsiku lonse;

koma wolungama amapatsa osamana.

27 Nsembe ya oipa inyansa;

makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.

28 Mboni yonama idzafa;

koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika.

29 Munthu woipa aumitsa nkhope yake;

koma woongoka mtima akonza njira zake.

30 Kulibe nzeru ngakhale luntha

ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.

31 Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo;

koma wopulumutsa ndiye Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/21-bf18b07f5d70f5c7c7a8eabca72c35d8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *