1 Wosauka woyenda mwangwiro
aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.
2 Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino;
ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.
3 Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake;
mtima wake udandaula pa Yehova.
4 Chuma chionjezetsa mabwenzi ambiri;
koma mnzake wa waumphawi amleka.
5 Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa;
wolankhula mabodza sadzapulumuka.
6 Ambiri adzapembedza waufulu;
ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.
7 Abale onse a wosauka amuda;
nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye?
Awatsata ndi mau, koma kuli zii.
8 Wolandira nzeru akonda moyo wake;
wosunga luntha adzapeza zabwino.
9 Mboni yonama sidzapulumuka chilango;
wolankhula mabodza adzaonongeka.
10 Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka;
nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi?
11 Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo;
ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.
12 Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango;
koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.
13 Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake;
ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.
14 Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate;
koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.
15 Ulesi ugonetsa tulo tofa nato;
ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.
16 Wosunga lamulo asunga moyo wake;
wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa.
17 Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova;
adzambwezera chokoma chakecho.
18 Menya mwanako, chiyembekezero chilipo,
osafunitsa kumuononga.
19 Munthu waukali alipire mwini;
pakuti ukampulumutsa udzateronso.
20 Tamvera uphungu, nulandire mwambo,
kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.
21 Muli zolingalira zambiri m’mtima mwa munthu;
koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.
22 Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake;
ndipo wosauka apambana munthu wonama.
23 Kuopa Yehova kupatsa moyo;
wokhala nako adzakhala wokhuta;
zoipa sizidzamgwera.
24 Waulesi alonga dzanja lake m’mbale,
osalibwezanso kukamwa kwake.
25 Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera;
nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
26 Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai,
ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.
27 Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa,
leka kumva mwambo.
28 Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo;
m’kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa.
29 Akonzera onyoza chiweruzo,
ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/19-c425ba6bdcf12be7ad411a40b3222ef1.mp3?version_id=1068—