1 Malongosoledwe a mtima nga munthu;
koma mayankhidwe a lilime achokera kwa Yehova.
2 Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake;
koma Yehova ayesa mizimu.
3 Pereka zochita zako kwa Yehova,
ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.
4 Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao;
ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
5 Yense wonyada mtima anyansa Yehova;
zoonadi sadzapulumuka chilango.
6 Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi;
apatuka pa zoipa poopa Yehova.
7 Njira za munthu zikakonda Yehova
ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.
8 Zapang’ono, pokhala chilungamo,
ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.
9 Mtima wa munthu ulingalira njira yake;
koma Yehova ayendetsa mapazi ake.
10 Mau a mlauli ali m’milomo ya mfumu;
m’kamwa mwake simudzachita chetera poweruza.
11 Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova;
ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m’thumba.
12 Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu;
pakuti mpando wao wakhazikika ndi chilungamo.
13 Milomo yolungama ikondweretsa mafumu;
wonena zoongoka amkonda.
14 Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa;
wanzeru adzaukhulula.
15 M’kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo;
kukoma mtima kwake kunga mtambo wa mvula ya masika.
16 Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide,
kulandira luntha ndi kusankhika koposasiliva?
17 Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa;
wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.
18 Kunyada kutsogolera kuonongeka;
mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.
19 Kufatsa mtima ndi osauka
kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.
20 Wolabadira mau adzapeza bwino;
ndipo wokhulupirira Yehova adala.
21 Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera;
ndipo kukoma kwa milomo kuonjezera kuphunzira.
22 Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake;
koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru.
23 Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake,
nuphunzitsanso milomo yake.
24 Mau okoma ndiwo chisa cha uchi,
otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.
25 Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka,
koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.
26 Wantchito adzigwirira yekha ntchito;
pakuti m’kamwa mwake mumfulumiza.
27 Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa;
ndipo m’milomo mwake muli moto wopsereza.
28 Munthu wokhota amautsa makani;
kazitape afetsa ubwenzi.
29 Munthu wa chiwawa akopa mnzake,
namuyendetsa m’njira yosakhala bwino.
30 Wotsinzina ndiye aganizira zokhota;
wosunama afikitsa zoipa.
31 Imvi ndiyo korona wa ulemu,
idzapezedwa m’njira ya chilungamo.
32 Wosakwiya msanga aposa wamphamvu;
wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.
33 Maere aponyedwa pamfunga;
koma ndiye Yehova alongosola zonse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/16-0ed9dacf531d43cebd0ca0689d79c719.mp3?version_id=1068—