1 Wokonda mwambo akonda kudziwa;
koma wakuda chidzudzulo apulukira.
2 Yehova akomera mtima munthu wabwino;
koma munthu wa ziwembu amtsutsa.
3 Munthu sadzakhazikika ndi udyo,
muzu wa olungama sudzasunthidwa.
4 Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake;
koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.
5 Maganizo a olungama ndi chiweruzo;
koma uphungu wa oipa unyenga.
6 Mau a oipa abisalira mwazi;
koma m’kamwa mwa olungama muwalanditsa.
7 Oipa amagwa kuli zii;
koma banja la olungama limaimabe.
8 Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake;
koma wokhota mtima adzanyozedwa.
9 Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo,
aposa wodzikuza, amene asowa zakudya.
10 Wolungama asamalira moyo wa choweta chake;
koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.
11 Zakudya zikwanira wolima minda yake;
koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru.
12 Woipa akhumba chokodwa ndi amphulupulu;
koma muzu wa olungama umabala zipatso.
13 M’kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;
koma wolungama amatuluka m’mavuto.
14 Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m’kamwa mwake;
zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye.
15 Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake;
koma wanzeru amamvera uphungu.
16 Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa;
koma wanzeru amabisa manyazi.
17 Wolankhula ntheradi aonetsa chilungamo;
koma mboni yonama imanyenga.
18 Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;
koma lilime la anzeru lilamitsa.
19 Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;
koma lilime lonama likhala kamphindi.
20 Chinyengo chili m’mitima ya oganizira zoipa;
koma aphungu a mtendere amakondwa.
21 Palibe vuto lidzagwera wolungama;
koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.
22 Milomo yonama inyansa Yehova;
koma ochita ntheradi amsekeretsa.
23 Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;
koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24 Dzanja la akhama lidzalamulira;
koma waulesi adzakhala ngati kapolo.
25 Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;
koma mau abwino aukondweretsa.
26 Wolungama atsogolera mnzake;
koma njira ya oipa iwasokeretsa.
27 Waulesi samaotcha nyama yake anaigwira;
koma wolungama amalandira chuma chopambana cha anthu.
28 M’khwalala la chilungamo muli moyo;
m’njira ya mayendedwe ake mulibe imfa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/12-a208f60d659d30d94ba0fd02c30d5dc5.mp3?version_id=1068—