Zochitira miyambo
1 Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele.
2 Kudziwa nzeru ndi mwambo;
kuzindikira mau ozindikiritsa;
3 kulandira mwambo wakusamalira machitidwe,
chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika;
4 kuchenjeza achibwana,
kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;
5 kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;
ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;
6 kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake,
mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.
Munthu asalole oipa amchete
7 Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa;
opusa anyoza nzeru ndi mwambo.
8 Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,
ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;
9 pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako,
ndi mkanda pakhosi pako.
10 Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.
11 Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,
tilalire osachimwa opanda chifukwa;
12 tiwameze ali ndi moyo ngati manda,
ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;
13 tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake,
tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;
14 udzachita nafe maere,
tonse tidzakhala ndi chotengeramo chimodzi.
15 Mwananga, usayende nao m’njira;
letsa phazi lako ku mayendedwe ao;
16 pakuti mapazi ao athamangira zoipa,
afulumira kukhetsa mwazi.
17 Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe;
18 ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao.
19 Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere;
chilanda moyo wa eni ake.
Chenjezo la Nzeru
20 Nzeru ifuula panja;
imveketsa mau ake pabwalo;
21 iitana posonkhana anthu polowera pachipata;
m’mzinda inena mau ake,
22 Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu?
Onyoza ndi kukonda kunyoza,
opusa ndi kuda nzeru?
23 Tembenukani pamene ndikudzudzulani;
taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,
ndikudziwitsani mau anga.
24 Chifukwa ndaitana, ndipo munakana;
ndatambasula dzanja langa,
ndipo panalibe analabadira;
25 koma munapeputsa uphungu wanga wonse,
ndi kukana kudzudzula kwanga.
26 Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu,
ndidzatonyola pakudza mantha anu;
27 pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,
ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu;
pakudza kwa inu vuto ndi nsautso.
28 Pamenepo adzandiitana,
koma sindidzavomera;
adzandifunatu, osandipeza ai;
29 chifukwa anada nzeru,
sanafune kuopa Yehova;
30 anakana uphungu wanga,
nanyoza kudzudzula kwanga konse;
31 momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,
nadzakhuta zolingalira zao.
32 Pakuti kubwerera m’mbuyo kwa achibwana kudzawapha;
ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
33 Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,
nadzakhala phee osaopa zoipa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PRO/1-32cef618ad9ecae5edf89bcb3338ccd7.mp3?version_id=1068—