Categories
MIKA

MIKA 5

1 Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.

Aneneratu za kubadwa kwa woweruza mu Israele

2 Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng’ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.

3 Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.

4 Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.

5 Ndipo ameneyo adzakhala mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m’dziko lathu, ndi pamene adzaponda m’zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.

6 Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m’dziko lathu, pamene aponda m’kati mwa malire athu.

7 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu.

8 Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwaamitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.

9 Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.

10 Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m’kati mwako, ndi kutha magaleta ako;

11 ndipo ndidzaononga mizinda ya m’dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;

12 ndipo ndidzaononga zanyanga za m’dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;

13 ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako.

14 Ndipo ndidzazula zifanizo zako m’kati mwako, ndi kutha mizinda yako.

15 Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera chilango mu mkwiyo waukali.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MIC/5-0ec30371f0ae0a7cdc9963307c21cf90.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *