Yesu achiritsa wakhate
1 Ndipo pakutsika pake paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu.
2 Ndipo onani, wakhateanadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.
3 Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.
4 Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.
Kenturiyo wa ku Kapernao
5 Ndipo m’mene Iye analowa mu Kapernao anadza kwa Iyekenturiyo, nampemba Iye,
6 nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m’nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa.
7 Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye.
8 Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.
9 Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita.
10 Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.
11 Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum’mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;
12 koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
13 Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
Mpongozi wa Petro
14 Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.
15 Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
16 Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;
17 kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesayamneneri, kuti,
Iye yekha anatenga zofooka zathu,
nanyamula nthenda zathu.
Matsatidwe ake a Yesu
18 Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamuliraophunziraamuke kutsidya lina.
19 Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako.
20 Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zao, komaMwana wa Munthualibe potsamira mutu wake.
21 Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine ndiyambe ndamuka kuika maliro a atate wanga.
22 Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.
Yesu aletsa namondwe
23 Ndipo pamene Iye atalowa m’ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye.
24 Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m’tulo.
25 Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika.
26 Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang’ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.
27 Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Ogwidwa ndi ziwanda a ku Gadara
28 Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu panjira imeneyo.
29 Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?
30 Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya.
31 Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m’gulu la nkhumbazo.
32 Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m’nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m’nyanjamo, ndipo linafa m’madzi.
33 Koma akuziweta anathawa, namuka kumzinda, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja.
34 Ndipo onani, mzinda wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m’mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m’malire ao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/8-a5ffb0a35c1132199afbfc101155b8e0.mp3?version_id=1068—