Categories
MATEYU

MATEYU 4

Yesu ayesedwa m’chipululu

1 Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi.

2 Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.

3 Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.

4 Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa,

Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha,

koma ndi mau onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.

5 Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,

6 nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti,

Adzalamulaangeloake za iwe,

ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe,

ungagunde konse phazi lako pamwala.

7 Yesu ananena naye,

Ndiponso kwalembedwa,

Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

8 Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;

9 nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.

10 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, ChokaSatana, pakuti kwalembedwa,

Ambuye Mulungu wako udzamgwadira,

ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.

11 Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.

Yesu mu Galileya. Ophunzira oyamba

12 Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;

13 ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m’malire a Zebuloni ndi Nafutali:

14 kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesayamneneri, kuti,

15 Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,

njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani,

Galileya wa anthu akunja,

16 anthu akukhala mumdima

adaona kuwala kwakukulu,

ndi kwa iwo okhala m’malo a mthunzi wa imfa,

kuwala kunatulukira iwo.

17 Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

18 Ndipo pamene Yesu analikuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m’nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.

19 Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

20 Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.

21 Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m’ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.

22 Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.

Yesu aphunzitsa, nalalika, nachiritsa

23 Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m’masunagogemwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.

24 Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.

25 Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi kuYerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/4-7eb8ec56f14f23a9494a1c6e35ca3ddc.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *