Yesu auka kwa akufa
1 Ndipo popita tsiku laSabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda.
2 Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakutimngelowa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.
3 Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala;
4 ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa.
5 Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa.
6 Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m’mene anagonamo Ambuye.
7 Ndipo pitani msanga, muuzeophunziraake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.
8 Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake.
9 Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira.
10 Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Mau omveka mwa Ayuda
11 Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.
12 Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri,
13 nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m’mene ife tinali m’tulo.
14 Ndipo ngati ichi chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa.
15 Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.
Yesu aoneka mu Galileya
16 Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira.
17 Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika.
18 Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
19 Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:
20 ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/28-cc01068682d7a153971601df37171ede.mp3?version_id=1068—