Fanizo la anamwali asanu ochenjera ndi asanu opusa
1 Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati.
2 Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera.
3 Pakuti opusawo, m’mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta;
4 koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.
5 Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.
6 Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! Tulukani kukakomana naye.
7 Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao.
8 Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima.
9 Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.
10 Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.
11 Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, mbuye, mutitsegulire ife.
12 Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.
13 Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.
Fanizo la ndalama za matalente
14 Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.
15 Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.
16 Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.
17 Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri.
18 Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake.
19 Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi.
20 Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu.
21 Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.
22 Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri.
23 Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m’chikondwerero cha mbuye wako.
24 Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze;
25 ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo.
26 Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze;
27 chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake.
28 Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.
29 Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho.
30 Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Moyo wosatha ndi kulanga kosatha
31 Koma pameneMwana wa Munthuadzadza mu ulemerero wake, ndiangeloonse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:
32 ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;
33 nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.
34 Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:
35 pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;
36 wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.
37 Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani?
38 Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani?
39 Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?
40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi Ine.
41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:
42 pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatse Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetse Ine:
43 ndinali mlendo, ndipo simunandilandire Ine; wamaliseche ndipo simunandiveke Ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simunadze kundiona Ine.
44 Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m’nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?
45 Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang’onong’ono, munalibe kundichitira ichi Ine.
46 Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/25-07908513c1ca256cdd1c96486b4e26f5.mp3?version_id=1068—