Categories
MATEYU

MATEYU 10

Atumwi khumi ndi awiri ndi utumiki wao

1 Ndipo pamene Iye anadziitaniraophunziraake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.

2 Ndipo maina ao aatumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake;

3 Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyuwamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;

4 Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye.

5 Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m’mudzi waAsamariyamusamalowamo:

6 koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israele.

7 Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

8 Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere.

9 Musadzitengere ndalama zagolide, kapena zasiliva, kapena zakobiri m’malamba mwanu;

10 kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.

11 Ndipo m’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.

12 Ndipo polowa m’nyumba muwalonjere.

13 Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.

14 Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu.

15 Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.

16 Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.

17 Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kubwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m’masunagogemwao;

18 ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.

19 Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo;

20 pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.

21 Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.

22 Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.

23 Koma pamene angakuzunzeni inu m’mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikiraMwana wa Munthuatadza.

24 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena kapolo saposa mbuye wake.

25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banjaBelezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?

26 Chifukwa chake musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanavundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika.

27 Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m’khutu, muchilalikire pa matsindwi a nyumba.

28 Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.

29 Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:

30 komatu inu, matsitsi onse a m’mutu mwanu awerengedwa.

31 Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.

32 Chifukwa chake yense amene adzavomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

33 Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

34 Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere padziko lapansi; sindinadzere kuponya mtendere, koma lupanga.

35 Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake:

36 ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake.

37 Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.

38 Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine.

39 Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza.

40 Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine.

41 Iye wakulandiramneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama adzalandira mphotho ya munthu wolungama.

42 Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang’ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAT/10-20c276684c3e365e4054681ffae4d9ca.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *