Davide apempha Mulungu kolimba amlanditse
Pemphero la Davide.
1 Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe;
pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi.
2 Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;
Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.
3 Mundichitire chifundo, Ambuye;
pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.
4 Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;
pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.
5 Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,
ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
6 Tcherani khutu pemphero langa, Yehova;
nimumvere mau a kupemba kwanga.
7 Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;
popeza mudzandivomereza.
8 Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;
ndipo palibe ntchito zonga zanu.
9 Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye;
nadzalemekeza dzina lanu.
10 Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa;
Inu ndinu Mulungu, nokhanu.
11 Mundionetse njira yanu, Yehova;
ndidzayenda m’choonadi chanu,
muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
12 Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga,
ndi mtima wanga wonse;
ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
13 Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu;
ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
14 Mulungu, odzikuza andiukira,
ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga,
ndipo sanaike Inu pamaso pao.
15 Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo,
wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
16 Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo;
mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu,
ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Mundichitire chizindikiro choti chabwino;
kuti ondida achione, nachite manyazi,
popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/86-c3329e477997094a5e689f1421a56f9d.mp3?version_id=1068—