Akumbutsa Mulungu madalitso akale, apempha awabwereze
Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la ana a Kora.
1 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova;
munabweza ukapolo wa Yakobo.
2 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu,
munafotsera zolakwa zao zonse.
3 Munabweza kuzaza kwanu konse;
munabwerera kumkwiyo wanu wotentha.
4 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu,
nimuletse udani wanu wa pa ife.
5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?
Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?
6 Kodi simudzatipatsanso moyo,
kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?
7 Tionetseni chifundo chanu, Yehova,
tipatseni chipulumutso chanu.
8 Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova;
pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake,
ndi okondedwa ake;
koma asabwererenso kuchita zopusa.
9 Indedi chipulumutso chake chili pafupi
ndi iwo akumuopa Iye;
kuti m’dziko mwathu mukhale ulemu.
10 Chifundo ndi choonadi zakomanizana;
chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.
11 Choonadi chiphukira m’dziko;
ndi chilungamo chasuzumira chili m’mwamba.
12 Inde Yehova adzapereka zokoma;
ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.
13 Chilungamo chidzamtsogolera;
ndipo chidzamkonzera mapazi ake njira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/85-c4c844fc1b8f723f7281b828236e7378.mp3?version_id=1068—