Categories
MASALIMO

MASALIMO 84

Okhala m’nyumba ya Yehova ndiwo amwai

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Gititi; Salimo la ana a Kora.

1 Pokhala Inu mpotikonda ndithu,

Yehova wa makamu!

2 Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova;

mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.

3 Mbawanso inapeza nyumba,

ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake,

pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu,

mfumu yanga ndi Mulungu wanga.

4 Odala iwo akugonera m’nyumba mwanu;

akulemekezani chilemekezere.

5 Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu;

mumtima mwake muli makwalala a kuZiyoni.

6 Popyola chigwa cha kulira misozi achiyesa cha akasupe;

inde mvula ya chizimalupsa ichidzaza ndi madalitso.

7 Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu,

aoneka pamaso pa Mulungu muZiyoni.

8 Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa.

Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo.

9 Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu;

ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.

10 Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma

koposa masiku ambirimbiri akukhala pena.

Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga,

kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.

11 Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa;

Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero;

sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

12 Yehova wa makamu,

wodala munthu wakukhulupirira Inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/84-e7d9f9ab67bd1354cd497363362f5251.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *