Categories
MASALIMO

MASALIMO 74

Malo oyera adetsedwa. Apempha Mulungu akumbuke chipangano chao

Chilangizo cha Asafu.

1 Mulungu, munatitayiranji chitayire?

Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?

2 Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale,

umene munauombola ukhale fuko la cholowa chanu;

Phiri laZiyonilimene mukhalamo.

3 Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha,

zoipa zonse adazichita mdani m’malo opatulika.

4 Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu;

aika mbendera zao zikhale zizindikiro.

5 Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango.

6 Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zake zonse

ndi nkhwangwa ndi nyundo.

7 Anatentha malo anu opatulika;

anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu.

8 Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi;

anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m’dzikomo.

9 Sitiziona zizindikiro zathu;

palibensomneneri;

ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.

10 Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu?

Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?

11 Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu?

Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu.

12 Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale,

wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi.

13 Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu;

mudaswa mitu ya zoopsa za m’madzi.

14 Mudaphwanya mitu yaLeviyatani;

mudampereka akhale chakudya cha zilombo za m’chipululu.

15 Mudagawa kasupe ndi mtsinje;

mudaphwetsa mitsinje yaikulu.

16 Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu,

munakonza kuunika ndi dzuwa.

17 Munaika malekezero onse a dziko lapansi;

munalenga dzinja ndi malimwe.

18 Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza,

ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

19 Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo;

musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse.

20 Samalirani chipanganocho;

pakuti malo a mdima a m’dziko adzala ndi zokhalamo chiwawa.

21 Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi;

wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu.

22 Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha;

kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.

23 Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu;

kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/74-f6b2ca6dd029419aab82d250c90fd897.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *