Nkhalamba idzaponya kwa Mulungu amene anamkhulupirira kuyambira ubwana wake
1 Ndikhulupirira Inu, Yehova.
Ndisachite manyazi nthawi zonse.
2 Ndikwatuleni m’chilungamo chanu, ndi kundilanditsa,
nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3 Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;
mwalamulira kundipulumutsa;
popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
4 Ndilanditseni, Mulungu wanga, m’dzanja la woipa,
m’dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.
5 Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova;
mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.
6 Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe,
kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu;
ndidzakulemekezani kosalekeza.
7 Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri;
koma Inu ndinu pothawira panga polimba.
8 M’kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu,
ndi ulemu wanu tsiku lonse.
9 Musanditaye mu ukalamba wanga;
musandisiye, pakutha mphamvu yanga.
10 Pakuti adani anga alankhula za ine;
ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,
11 ndi kuti, Wamsiya Mulungu.
Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa.
12 Musandikhalire kutali, Mulungu;
fulumirani kundithandiza, Mulungu.
13 Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe;
chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa.
14 Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,
ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.
15 Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu,
ndi chipulumutso chanu tsiku lonse;
pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.
16 Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova;
ndidzatchula chilungamo chanu, inde chanu chokha.
17 Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga;
ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu.
18 Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu;
kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu,
mphamvu yanu kwa onse akudza m’mbuyo.
19 Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo;
Inu amene munachita zazikulu,
akunga Inu ndani, Mulungu?
20 Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa,
mudzatipatsanso moyo,
ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
21 Mundionjezere ukulu wanga,
ndipo munditembenukire kundisangalatsa.
22 Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa,
kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga;
ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze,
ndinu Woyerayo wa Israele.
23 Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo;
inde, moyo wanga umene munaombola.
24 Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse,
pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/71-0771d2c3ef063cd4dd268f590b828ffa.mp3?version_id=1068—