Adani amzinga, Davide adziponya kwa Mulungu
Syigayoni wa Davide woimbira Yehova, chifukwa cha mau a Kusi Mbenjamini.
1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu;
mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;
2 kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,
ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.
3 Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi;
ngati m’manja anga muli chosalungama;
4 ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine;
(inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);
5 mdani alondole moyo wanga, naupeze;
naupondereze pansi moyo wanga,
naukhalitse ulemu wanga m’fumbi.
6 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,
nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa;
ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.
7 Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;
ndipo pamwamba pao mubwerere kunka kumwamba.
8 Yehova aweruza anthu mlandu;
mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa,
ndi ungwiro wanga uli mwa ine.
9 Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani,
koma wolungamayo mumkhazikitse.
Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
10 Chikopa changa chili ndi Mulungu,
wopulumutsa oongoka mtima.
11 Mulungu ndiye Woweruza wolungama,
ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.
12 Akapanda kutembenuka munthu,
iye adzanola lupanga lake;
wakoka uta wake, naupiringidza.
13 Ndipo anamkonzera zida za imfa;
mivi yake aipanga ikhale yansakali.
14 Taonani, ali m’chikuta cha zopanda pake;
anaima ndi chovuta, nabala bodza.
15 Anachita dzenje, nalikumba,
nagwa m’mbuna yomwe anaikumba.
16 Chovuta chake chidzambwerera mwini,
ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.
17 Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake;
ndipo ndidzaimbira Yehova Wam’mwambamwamba.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/7-a085905e3182f7625fd62b99645e6371.mp3?version_id=1068—