Achenjeza onse alemekeze Mulungu pa ntchito zake zodabwitsa
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Nyimbo, Salimo.
1 Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.
2 Imbirani ulemerero wa dzina lake;
pomlemekeza mumchitire ulemerero.
3 Nenani kwa Mulungu, Ha,
ntchito zanu nzoopsa nanga!
Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.
4 Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,
ndipo lidzakuimbirani;
ndzaimbira dzina lanu.
5 Idzani, muone ntchito za Mulungu;
zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.
6 Anasanduliza nyanja ikhale mtunda.
Anaoloka mtsinje choponda pansi,
apo tinakondwera mwa Iye.
7 Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha;
maso ake ayang’aniraamitundu;
opikisana ndi Iye asadzikuze.
8 Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,
ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake.
9 Iye amene asunga moyo wathu tingafe,
osalola phazi lathu literereke.
10 Pakuti munatiyesera, Mulungu,
munatiyenga monga ayengasiliva.
11 Munapita nafe kuukonde;
munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.
12 Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;
tinapyola moto ndi madzi;
koma munatifikitsa potitsitsimutsa.
13 Ndidzalowa m’nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,
ndidzakuchitirani zowinda zanga,
14 zimene inazitchula milomo yanga,
ndinazinena pakamwa panga posautsika ine.
15 Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona,
pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa;
ndidzakonza ng’ombe pamodzi ndi mbuzi.
16 Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,
ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.
17 Ndinamfuulira Iye pakamwa panga,
ndipo ndinamkuza ndi lilime langa.
18 Ndikadasekera zopanda pake m’mtima mwanga,
Ambuye sakadamvera.
19 Koma Mulungu anamvadi;
anamvera mau a pemphero langa.
20 Wolemekezeka Mulungu,
amene sanandipatutsire ine pemphero langa,
kapena chifundo chake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/66-cd2c9e7202df993c36a1484f8905c376.mp3?version_id=1068—