Madandaulo ndi pempho la Davide
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri.
1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;
mwakwiya; tibwezereni.
2 Mwagwedeza dziko, mwaling’amba.
Konzani ming’alu yake; pakuti ligwedezeka.
3 Mwaonetsa anthu anu zowawa,
mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.
4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,
aikweze chifukwa cha choonadi.
5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,
pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.
6 Mulungu walankhula m’chiyero chake; ndidzakondwerera,
ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.
7 Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;
ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga;
Yuda ndiye wolamulira wanga.
8 Mowabu ndiye mkhate wanga;
pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga.
Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.
9 Adzandifikitsa ndani m’mzinda wa m’linga?
Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
10 Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya?
Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.
11 Tithandizeni kunsautso;
kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.
12 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima,
ndipo Iye adzapondereza otisautsa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/60-396c9720e403cdadaf93d7346d326fac.mp3?version_id=1068—