Davide apempha chifundo kwa Mulungu
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto, pa Seminiti. Salimo la Davide.
1 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
ndipo musandilange muukali wanu.
2 Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine.
Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu;
ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?
4 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;
ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.
5 Pakuti muimfa m’mosakumbukira Inu;
m’mandamo adzakuyamikani ndani?
6 Ndalema nako kuusa moyo kwanga;
ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;
mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
7 Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni;
lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa.
8 Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake;
pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga.
9 Wamva Yehova kupemba kwanga;
Yehova adzalandira pemphero langa.
10 Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu
adani anga onse;
adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/6-12e6ac2c0a2d65440fbb65d805f91b7a.mp3?version_id=1068—