Categories
MASALIMO

MASALIMO 57

Davide apempha Mulungu amtchinjirize, namlemekezapo

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Altasheti. Mikitamu wa Davide; muja anathawa Saulo, ali m’phanga.

1 Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo;

pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu,

ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu,

kufikira zosakazazo zidzapita.

2 Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam’mwambamwamba;

ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.

3 Adzanditumizira m’mwamba, nadzandipulumutsa

ponditonza wofuna kundimeza;

Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.

4 Moyo wanga uli pakati pa mikango;

ndigona pakati pa oyaka moto,

ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi,

ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.

5 Mukwezeke m’mwambamwamba, Mulungu;

ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.

6 Ananditchera ukonde apo ndiyenda;

moyo wanga wawerama.

Anandikumbira mbuna patsogolo panga;

anagwa m’kati mwake iwo okha.

7 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;

ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.

8 Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze!

Ndidzauka ndekha mamawa.

9 Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye,

ndidzakuimbirani mwa mitundu.

10 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m’mwamba,

ndi choonadi chanu kufikira mitambo.

11 Kwezekani m’mwambamwamba, Mulungu;

ulemerero wanu ukhale pamwamba m’dziko lonse lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/57-b8e32b44aecaea2420ecc0fbf388b73f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *