Davide apempha Mulungu amlanditse; ayamika atamlanditsa
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Yonat-Elem-Rekokimu. Mikitamu wa Davide; muja Afilisti anamgwira mu Gati.
1 Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza.
Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.
2 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse,
pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.
3 Tsiku lakuopa ine,
ndidzakhulupirira Inu.
4 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake,
ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;
anthu adzandichitanji?
5 Tsiku lonse atenderuza mau anga,
zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.
6 Amemezana, alalira,
atchereza mapazi anga,
popeza alindira moyo wanga.
7 Kodi adzapulumuka ndi zopanda pake?
Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.
8 Muwerenga kuthawathawa kwanga,
sungani misozi yanga m’nsupa yanu;
kodi siikhala m’buku mwanu?
9 Pamenepo adani anga adzabwerera m’mbuyo tsiku lakuitana ine.
Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.
10 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake,
mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake.
11 Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;
munthu adzandichitanji?
12 Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine,
ndidzakuchitirani zoyamika.
13 Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa,
simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?
Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu
m’kuunika kwa amoyo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/56-87c25ca541a0a6dc7b071d0a07c0ab37.mp3?version_id=1068—