Categories
MASALIMO

MASALIMO 55

Davide adandaula pa kuipa kwa adani, adziponya kwa Mulungu, nalangiza ena azitero iwo omwe

Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Neginoto. Chilangizo cha Davide.

1 Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu;

ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.

2 Mverani, ndipo mundiyankhe,

ndiliralira m’kudandaula kwanga ndi kubuula;

3 chifukwa cha mau a mdani,

chifukwa cha kundipsinja woipa;

pakuti andisenza zopanda pake,

ndipo adana nane mumkwiyo.

4 Mtima wanga uwawa m’kati mwanga;

ndipo zoopsa za imfa zandigwera.

5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,

ndipo zoopsetsa zandikuta.

6 Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa!

Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.

7 Onani, ndikadathawira kutali,

ndikadagona m’chipululu.

8 Ndikadafulumira ndipulumuke

kumphepo yolimba ndi namondwe.

9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao,

pakuti ndaona chiwawa ndi ndeu m’mzindamo.

10 Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku;

ndipo m’kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta.

11 M’kati mwake muli kusakaza,

chiwawa ndi chinyengo sizichoka m’makwalala ake.

12 Pakuti si mdani amene ananditonzayo;

pakadatero ndikadachilola,

amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;

pakadatero ndikadambisalira:

13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,

tsamwali wanga, wodziwana nane.

14 Tinapangirana upo wokoma,

tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu.

15 Imfa iwagwere modzidzimutsa,

atsikire kumanda ali amoyo,

pakuti m’mokhala mwao muli zoipa pakati pao.

16 Koma ine ndidzafuulira kwa Mulungu;

ndipo Yehova adzandipulumutsa.

17 Madzulo, m’mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,

ndipo adzamva mau anga.

18 Anaombola moyo wanga kunkhondo,

ndikhale mumtendere,

pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa,

ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe.

Popeza iwowa sasinthika konse,

ndipo saopa Mulungu.

20 Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye,

anaipsa pangano lake.

21 Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka,

koma mumtima mwake munali nkhondo,

mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga,

koma anali malupanga osololasolola.

22 Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza,

nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

23 Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko.

Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu;

koma ine ndidzakhulupirira Inu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/55-f6f43717a2860f3b667923d0cea61273.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *