Mtima wolira kuyanjana ndi Mulungu mu Kachisi
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora.
1 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;
motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
2 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu,
la kwa Mulungu wamoyo.
Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
3 Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa,
usana ndi usiku;
pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,
Mulungu wako ali kuti?
4 Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m’kati mwa ine,
pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu,
ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu,
ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika,
ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?
Ndi kuzingwa m’kati mwanga?
Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso
chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
6 Mulungu wanga, moyo wanga
udziweramira m’kati mwanga;
chifukwa chake ndikumbukira Inu m’dziko la Yordani,
ndi mu Aheremoni, m’kaphiri ka Mizara.
7 Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,
pa mkokomo wa matiti anu;
mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
8 Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake,
ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine.
Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
9 Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa,
mwandiiwala chifukwa ninji?
Ndimayenderanji wakulira
chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?
10 Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga;
pakunena ndine dzuwa lonse,
Mulungu wako ali kuti?
11 Udziweramiranji moyo wanga iwe?
Ndi kuzingwa m’kati mwanga?
Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,
ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/42-ae42dc50afb061e3a3a74ad4c3630ce9.mp3?version_id=1068—