Mulungu adalitsa wosamalira osauka. Adani ndi mabwenzi amchitira Davide zoipa, Mulungu amlanditse
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.
1 Wodala iye amene asamalira wosauka!
Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.
2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo,
ndipo adzadalitsika padziko lapansi,
ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake.
3 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;
podwala iye mukonza pogona pake.
4 Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova;
Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu.
5 Adani anga andinenera choipa, ndi kuti,
adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?
6 Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;
mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake,
akanka nayenda namakanena.
7 Onse akudana nane andinong’onezerana;
apangana chondiipsa ine.
8 Chamgwera chinthu choopsa, ati;
popeza ali gonire sadzaukanso.
9 Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira,
ndiye amene adadyako mkate wanga,
anandikwezera chidendene chake.
10 Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse,
kuti ndiwabwezere.
11 Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine,
popeza mdani wanga sandiseka.
12 Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga,
ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.
13 Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele,
kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.
Amen, ndi Amen.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/41-537b08f0cc93ae7eeaae58059123a735.mp3?version_id=1068—