Categories
MASALIMO

MASALIMO 37

Kusangalala kwa ochimwa kudzatha, olungama akhalitsa nathandizidwa ndi Mulungu

Salimo la Davide.

1 Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa,

usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.

2 Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,

ndipo adzafota monga msipu wauwisi.

3 Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma;

khala m’dziko, ndipo tsata choonadi.

4 Udzikondweretsenso mwa Yehova;

ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

5 Pereka njira yako kwa Yehova;

khulupiriranso Iye, adzachichita.

6 Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika,

ndi kuweruza kwako monga usana.

7 Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye;

usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m’njira yake,

chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.

8 Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo;

usavutike mtima ungachite choipa.

9 Pakuti ochita zoipa adzadulidwa;

koma iwo akuyembekeza Yehova,

iwowa adzalandira dziko lapansi.

10 Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti;

inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.

11 Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;

nadzakondwera nao mtendere wochuluka.

12 Woipa apangira chiwembu wolungama,

namkukutira mano.

13 Ambuye adzamseka,

popeza apenya kuti tsiku lake likudza.

14 Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;

alikhe ozunzika ndi aumphawi,

aphe amene ali oongoka m’njira.

15 Lupanga lao lidzalowa m’mtima mwao momwe,

ndipo mauta ao adzathyoledwa.

16 Zochepa zake za wolungama zikoma

koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.

17 Pakuti manja a oipa adzathyoledwa,

koma Yehova achirikiza olungama.

18 Yehova adziwa masiku a anthu angwiro;

ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha.

19 Sadzachita manyazi m’nyengo yoipa,

ndipo m’masiku a njala adzakhuta.

20 Pakuti oipa adzatayika,

ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa;

adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.

21 Woipa akongola, wosabweza,

koma wolungama achitira chifundo, napereka.

22 Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;

koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.

23 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;

ndipo akondwera nayo njira yake.

24 Angakhale akagwa, satayikiratu,

pakuti Yehova agwira dzanja lake.

25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba;

ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa,

kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

26 Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa;

ndipo mbumba zake zidalitsidwa.

27 Siyana nacho choipa, nuchite chokoma,

nukhale nthawi zonse.

28 Pakuti Yehova akonda chiweruzo,

ndipo sataya okondedwa ake.

Asungika kosatha,

koma adzadula mbumba za oipa.

29 Olungama adzalandira dziko lapansi,

nadzakhala momwemo kosatha.

30 Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,

ndi lilime lake linena chiweruzo.

31 Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake;

pakuyenda pake sadzaterereka.

32 Woipa aunguza wolungama,

nafuna kumupha.

33 Yehova sadzamsiya m’dzanja lake;

ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.

34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yake,

ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko.

Pakudulidwa oipa udzapenya.

35 Ndapenya woipa, alikuopsa,

natasa monga mtengo wauwisi wanzika.

36 Koma anapita ndipo taona, kwati zii;

ndipo ndinampwaira osampeza.

37 Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!

Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.

38 Koma olakwa adzaonongeka pamodzi;

matsiriziro a oipa adzadulidwa.

39 Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova,

Iye ndiye mphamvu yao m’nyengo ya nsautso.

40 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa;

awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa,

chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/37-b05a1f859375b97fcce3087bbc69abe3.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *