Kukhulupirika kwa Mulungu
Salimo la Davide, muja anathawa Abisalomu mwana wake.
1 Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine!
Akundiukira ine ndi ambiri.
2 Ambiri amati kwa moyo wanga,
alibe chipulumutso mwa Mulungu.
3 Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa;
ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
4 Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga,
ndipo andiyankha m’phiri lake loyera.
5 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;
ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza.
6 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.
7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!
Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;
mwawathyola mano oipawo.
8 Chipulumutso ncha Yehova;
dalitso lanu likhale pa anthu anu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/3-60f1eca1f3eec23e92384018de71d6bc.mp3?version_id=1068—