Apempha chipulumutso, ayamika populumutsidwa
Salimo la Davide.
1 Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira;
thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva;
pakuti ngati munditontholera ine,
ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
2 Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu,
pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.
3 Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa,
ndi ochita zopanda pake;
amene alankhula zamtendere ndi anansi ao,
koma mumtima mwao muli choipa.
4 Muwapatse monga mwa ntchito zao,
ndi monga mwa choipa chochita iwo;
muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao;
muwabwezere zoyenera iwo.
5 Pakuti sasamala ntchito za Yehova,
kapena machitidwe a manja ake,
adzawapasula, osawamanganso.
6 Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa;
mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza,
chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu;
ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
8 Yehova ndiye mphamvu yao,
inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake.
9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu;
muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/28-18f7c07f0c5a257e43abf9589f958ea2.mp3?version_id=1068—